Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Khalanibe Ofatsa Mukapanikizika na Mayeso

Khalanibe Ofatsa Mukapanikizika na Mayeso

Kufatsa kwa Mose kunayesedwa pamene Aisiraeli anali kukangana naye komanso pamene anapanikizika maganizo (Num. 20:2-5; w19.02 12 ¶19)

Panthawiyi, Mose analephela kukhala wofatsa (Num. 20:10; w19.02 13 ¶20-21)

Yehova analanga Mose na Aroni cifukwa ca colakwa cacikulu cimene anacita (Num. 20:12; w09 9/1 19 ¶5)

Munthu wofatsa sakwiya msanga, sakhala wodzikuza, kapena wonyada. Ngakhale pamene ena amukhumudwitsa, amapilila moleza mtima, sakwiya, sasunga cakukhosi, kapena kubwezela.