Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CITANI KHAMA PA ULALIKI | WONJEZELANI CIMWEMWE CANU MU ULALIKI

Seŵenzetsani Mawu a Mulungu

Seŵenzetsani Mawu a Mulungu

Mawu a Mulungu ni amphamvu! (Aheb. 4:12) Angafike pamtima ngakhale anthu amene sadziŵa Mulungu. (1 Ates. 1:9; 2:13) Timapeza cimwemwe cacikulu ngati winawake wakondwela na mfundo inayake ya coonadi ca m’Baibo imene tamuonetsa.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI PEZANI CIMWEMWE PA NCHITO YOPANGA OPHUNZILA—NOLANI MALUSO ANU—LOLANI MPHAMVU YA MAWU A MULUNGU KUGWILA NCHITO, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AWA:

  • Kodi mlongo Neeta walola bwanji mphamvu ya Mawu a Mulungu kugwila nchito pothandiza Rose kuona kufunika kofufuza m’Mawu a Mulungu?

  • Kodi Neeta walola bwanji mphamvu ya Mawu a Mulungu kugwila nchito mwa kuŵelenga lemba mokweza na kufotokoza cabe mfundo yofunika pa lembalo?

  • N’ciani cimene cionetsa kuti lemba lamufika pamtima Rose? Nanga muona kuti zimenezi zamukhudza bwanji Neeta?