Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Sankhani Mabwenzi Mwanzelu

Sankhani Mabwenzi Mwanzelu

Zimene zinacitikila Aisiraeli m’cigwa ca Moabu, ni cenjezo kwa Akhristu lelolino. (1 Akor. 10:6, 8, 11) Aisiraeli amene anayamba kugwilizana na akazi aciwelewele komanso olambila mafano acimoabu, ananyengedwa mpaka kucita macimo aakulu. Izi zinabweletsa mavuto aakulu. (Num. 25:9) Nafenso timakhala pakati pa anthu osalambila Yehova, monga anzathu a kunchito, akusukulu, anansi athu, acibale athu, ndi anthu ena amene timadziŵana nawo. Kodi nkhani ya m’Baibo imeneyi itiphunzitsa ciani za kuopsa kopanga ubwenzi ndi anthu otelo?

ONELELANI VIDIYO YAKUTI ZITSANZO ZOTICENJEZA MASIKU ANO—KAMBALI KAKE, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Ni maganizo olakwika ati amene Zimiri ndi anthu ena anauza Yamini?

  • Kodi Pinihasi anamuthandiza bwanji Yamini kuona zinthu moyenela?

  • Kodi kucita zinthu mwaubwenzi na munthu wosakhulupilila n’kosiyana bwanji na kukhala naye pa ubwenzi?

  • N’cifukwa ciani tiyenela kusamala posankha mabwenzi apamtima ngakhale mumpingo?

  • N’cifukwa ciani tiyenela kupewa kuceza ndi anthu osawadziŵa bwino pamalo ocezela pa intaneti?