March 15-21
NUMERI 11-12
Nyimbo 46 na Pemphelo
Mawu Oyamba (Mph. 1)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“N’cifukwa Ciani Tiyenela Kupewa Mzimu Wodandaula?”: (Mph. 10)
Kufufuza Cuma Cauzimu: (Mph. 10)
Num. 11:7, 8—Kodi maonekedwe na makomedwe a mana zinaonetsa bwanji ubwino wa Yehova? (it-2 309)
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (Mph. 4) Num. 11:1-15 (th phunzilo 2)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Kuitanila Anthu ku Cikumbutso: (Mph. 3) Yambani na makambilano acitsanzo. Mwininyumba akaonetsa cidwi, chulani na kukambilana vidiyo yakuti Kukumbukila Imfa ya Yesu (koma musaitambitse). (th phunzilo 11)
Ulendo Wobwelelako: (Mph. 3) Citani ulendo wobwelelako kwa munthu amene anaonetsa cidwi ndipo analandila ciitanilo ca ku Cikumbutso. (th phunzilo 4)
Ulendo Wobwelelako: (Mph. 5) Pambuyo pa nkhani ya Cikumbutso, yambitsani makambilano na munthu wacidwi amene wapezeka pa Cikumbutso, ndipo yankhani funso limene wafunsa lokhudza pulogilamuyo. (th phunzilo 2)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Kodi Mukukonzekela Cikumbutso?”: (Mph. 15) Kukambilana. Pelekani zilengezo zilizonse zofunikila zokhudza makonzedwe a Cikumbutso. Onetsani vidiyo yakuti Mmene Mungapangile Mkate wa Cikumbutso.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (Mph. 30) lfb phunzilo 27
Mawu Othela (Mph. 3)
Nyimbo 123 na Pemphelo