Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Petulo na Yohane akukonzekela Pasika wa mu 33 C.E. m’cipinda capamwamba

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kodi Mukukonzekela Cikumbutso?

Kodi Mukukonzekela Cikumbutso?

Mwambo wothela wa Pasika umene Yesu anacita unali wapadela kwambili. Popeza anali pafupi kuphedwa, Yesu anakonza zakuti adye Pasika pamodzi na atumwi ake na kuyambitsa mwambo watsopano wapacaka, umene umachedwa Mgonelo wa Ambuye. Conco anatumiza Petulo na Yohane kuti akakonze cipinda codyelamo Pasika. (Luka 22:7-13; onani cithunzi pacikuto.) Izi zitikumbutsa kuti tiyenela kukonzekela Cikumbutso ca pa March 27. Mipingo iyenela kuti inapanga kale makonzedwe okhudza mlankhuli, ziphiphilitso, na zina zotelo. Koma n’ciani cimene aliyense wa ife angacite pokonzekela Cikumbutso?

Konzekeletsani mtima wanu. Ŵelengani na kusinkha-sinkha malemba oŵelenga pa nyengo ya Cikumbutso. Ndandanda mungaipeze m’kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku. Ndandanda yokhala na zambili imapezeka mu Buku Lothandiza Pophunzila Mawu a Mulungu, mutu 16. (Onaninso Kabuku ka Umoyo na Utumiki ka April 2020.) Mabanja angapeze nkhani zokambilana pa kulambila kwa pabanja zokhudza kufunika kwa dipo mwa kufufuza m’buku lakuti Watch Tower Publications Index kapena mu Buku Lofufuzila Nkhani la Mboni za Yehova.

Itanilani ena ku Cikumbutso. Tengankoni mbali mokwanila pa kampeni yomemeza anthu ku Cikumbutso. Ganizilani za anthu amene mungawaitanileko, monga anthu amene mumacitako maulendo obwelelako, maphunzilo anu a Baibo akale, anzanu, na acibale anu. Akulu ayenela kuyesetsa kuitanila ozilala ku Cikumbutso. Ngati munthu amakhala m’dela lina, mungapeze nthawi na malo kumene kudzacitikila Cikumbutso m’dela lake mwa kupita pa mbali yakuti ZOKHUDZA IFE pa tsamba loyamba la pa jw.org, na kusankha “Cikumbutso.”

N’ciani cina cimene tingacite pokonzekela Cikumbutso?