Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

N’cifukwa Ciani Tiyenela Kupewa Mzimu Wodandaula?

N’cifukwa Ciani Tiyenela Kupewa Mzimu Wodandaula?

Yehova sakondwela na mzimu wodandaula (Num. 11:1; w01 6/15 17 ¶20)

Mzimu wodandaula umaonetsa kuti munthu ni wodzikonda komanso wosayamikila (Num. 11:4-6; w06 7/15 15 ¶7)

Mzimu wodandaula umafooketsa ena (Num. 11:10-15; it-2 719 ¶4)

Ngakhale kuti Aisiraeli anakumana na mavuto ambili m’cipululu, anali na zifukwa zambili zokhalila oyamikila. Tingapewe mzimu wodandaula ngati nthawi zonse timaganizila madalitso amene Yehova watipatsa.