Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CITANI KHAMA PA ULALIKI | WONJEZELANI CIMWEMWE CANU MU ULALIKI

Funsani Mafunso

Funsani Mafunso

Yehova, “Mulungu wacimwemwe,” amafuna kuti tizipeza cimwemwe mu ulaliki. (1 Tim. 1:11) Cimwemwe cathu cimawonjezeka ngati tikulitsa maluso athu mu ulaliki. Kufunsa mafunso kumautsa cidwi ca munthu. Komanso ni njila yabwino yoyambitsila makambilano. Mafunso amalimbikitsa anthu kuganiza. (Mat. 22:41-45) Ngati tifunsa munthu mafunso na kumumvetsela, timakhala ngati tikumuuza kuti, ‘Ndiwe wofunika kwa ine.’ (Yak. 1:19) Mayankho amene munthu angapeleke angatithandize kudziŵa mmene tingakambile naye kuti timufike pa mtima.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI PEZANI CIMWEMWE PA NCHITO YOPANGA OPHUNZILA—NOLANI MALUSO ANU—KUFUNSA MAFUNSO, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Ni makhalidwe abwino ati amene Rose anaonetsa?

  • Kodi mlongo Neeta anaseŵenzetsa bwanji mafunso poonetsa cidwi kwa womvetsela wake?

  • Kodi Neeta anaseŵenzetsa bwanji mafunso pothandiza Rose kukulitsa cidwi comvetsela uthenga wabwino?

  • Kodi Neeta anagwilitsila nchito bwanji mafunso pothandiza Rose kuganizilapo pa zimene anali kukambilana naye?