Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Pewani Kutengela Anthu Osakhulupilika

Pewani Kutengela Anthu Osakhulupilika

Kora, Datani na Abiramu anaonetsa kusakhulupilika kwa Yehova mwa kupandukila makonzedwe ake. Yehova anawononga opandukawo na onse amene anali ku mbali yawo. (Num. 16:26, 27, 31-33) Ni zocitika monga ziti zimene zingayese kukhulupilika kwathu kwa Yehova? Ni zitsanzo ziti za m’Baibo zimene zingatithandize kuti tisatengele anthu osakhulupilika?

ONELELANI VIDIYO YAKUTI PEWANI KUTENGELA ANTHU OSAKHULUPILIKA, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Ni cocitika citi cimene cinayesa kukhulupilika kwa Nadi? Nanga ni citsanzo citi coticenjeza cimene cinamuthandiza kukhalabe wokhulupilika?

  • Ni cocitika cotani cimene cinayesa kukhulupilika kwa m’bale amene anakhumudwa? Nanga ni citsanzo citi coticenjeza cimene cinamuthandiza kukhalabe wokhulupilika?

  • N’ciani cinayesa kukhulupilika kwa m’bale Elliott? Nanga ni citsanzo citi coticenjeza cimene cinamuthandiza kukhalabe wokhulupilika?

  • N’ciani cinayesa kukhulupilika kwa m’bale wina kusukulu? Nanga ni citsanzo citi coticenjeza cimene cinamuthandiza kukhalabe wokhulupilika?