UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Mayeso Onse Ali na Mapeto Ake
Mayeso angatilefule mosavuta maka-maka ngati akhalitsa. Davide anadziŵa kuti ciyeso cake cocokela kwa Mfumu Sauli cidzatha m’kupita kwa nthawi, ndipo adzakhala mfumu monga mmene Yehova analonjezela. (1 Sam. 16:13) Cikhulupililo cake Davide cinam’thandiza kukhala woleza mtima na kuyembekezela Yehova.
Tikamayesedwa, mwina tingakwanitse kuthetsa vuto lathu cifukwa ca kucita zinthu mocenjela, kudziŵa zinthu, kapena cifukwa cokhala woganiza bwino. (1 Sam. 21:12-14; Miy. 1:4) Komabe, mavuto ena sangathe ngakhale kuti tacita zonse zotheka mogwilizana na mfundo za m’Baibo. Zikatelo, tiyenela kukhala oleza mtima na kuyembekezela Yehova. Posacedwa, iye adzathetsa mavuto athu onse, ndipo “adzapukuta misozi yonse” m’maso mwathu. (Chiv. 21:4) Kaya mavuto athu athe cifukwa cakuti Yehova waloŵelelapo kapena kaamba ka zifukwa zina, cimene sitikayikila n’cakuti: Mayeso onse ali na mapeto ake. Mfundo imeneyi ingatitonthoze.
ONELELANI VIDIYO YAKUTI ANTHU OGWILIZANA M’DZIKO LOGAŴIKANA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:
-
Ni zopinga zotani zimene Akhristu ena anakumana nazo kum’mwela kwa dziko la America?
-
Kodi anaonetsa bwanji kuleza mtima na cikondi?
-
Kodi anacita ciani kuti apitilize kuika maganizo awo pa “zinthu zofunika kwambili”?—Afil. 1:10