Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kodi Mabwenzi Anu a pa Intaneti ni Otani?

Kodi Mabwenzi Anu a pa Intaneti ni Otani?

Bwenzi ni munthu “amene amagwilizana kwambili na wina cifukwa cakuti amamukonda kapena kumulemekeza.” Mwacitsanzo, Yonatani na Davide anakhala pa ubwenzi wathithithi pambuyo pakuti Davide wapha Goliyati. (1 Sam. 18:1) Aliyense wa iwo anali na makhalidwe amene mnzake anali kukopeka nawo. Cotelo, kuti anthu akhale pa ubwenzi wolimba amafunika kudziŵana bwino. Kudziŵana na munthu wina kumatenga nthawi komanso kumafuna khama. Komabe, anthu angakhale “mabwenzi” pa masoshomidiya mwa kugodiniza batani inayake pa cipangizo cawo. Anthu pa Intaneti amakonzekela bwino zimene afuna kukamba, ndipo angathe kudzisintha. Conco zimakhala zosavuta kwa iwo kubisa umunthu wawo. N’cifukwa cake tiyenela kukhala osamala posankha mabwezi pa Intaneti. Musamaope kunyalanyaza kapena kukana, ngati anthu ena amene simuwadziŵa kwenikweni akupemphani kuti mukhale mabwenzi awo, poopa kuti mungawakhumudwitse. Podziŵilatu mavuto amene angakumane nawo, ena asankha kusaseŵenzetsa masoshomidiya. Koma kodi muyenela kukumbukila ciani mukasankha kuseŵenzetsa soshomidiya?

TAMBANI VIDIYO YAKUTI MUZISAMALA POCEZA NA ANTHU PA INTANETI, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AWA:

  • Kodi muyenela kuganizila ciani musanalembe ndemanga yanu kapena kuika zithunzi pa soshomidiya?

  • N’cifukwa ciani muyenela kusankha mosamala mabwenzi anu pa Intaneti?

  • N’cifukwa ciani muyenela kudziikila malile pa kuculuka kwa nthawi imene mumathela pa soshomidiya?—Aef. 5:15, 16