Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CITANI KHAMA PA ULALIKI

Makambilano Acitsanzo

Makambilano Acitsanzo

KUITANILA ANTHU KU CIKUMBUTSO (March 11–April 4)

“Ndife okondwa kukuitanilani ku cocitika capadela kumene kudzapezeka anthu mamiliyoni ambili. Cocitika cimeneci ni mwambo wokumbukila imfa ya Yesu.” Ndiyeno patsani munthuyo kapepala koitanila anthu ku Cikumbutso kopulinta kapena ka pacipangizo. “Kapepala aka ka ciitano kaonetsa nthawi na malo kumene cocitikaci cidzacitikile kwathu kuno. Tikuitanilaninso ku nkhani yapadela imene idzakambidwa kumapeto kwa mlungu woti cikumbutso cicitika mlungu wotsatila.”

Akaonetsa Cidwi: Muonetseni [kapena m’tumizileni pa meseji kapena pa imelo] vidiyo yakuti Kukumbukila Imfa ya Yesu.

Ulalo: N’cifukwa Ciyani Yesu Anafa?

ULENDO WOYAMBA (March 1-10, April 5-30)

Funso: Kodi Yesu Ndani?

Lemba: Mat. 16:16

Ulalo: N’cifukwa Ciyani Yesu Anafa?

ULENDO WOBWELELAKO

Funso: N’cifukwa Ciyani Yesu Anafa?

Lemba: Mat. 20:28

Ulalo: Kodi tingaonetse bwanji kuti timayamikila nsembe ya dipo la Yesu?