Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Cithunzi ca pacikuto: Mfumukazi ya ku Sheba yafika ku nyumba yacifumu ya Solomo

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Anaona Nzelu Kukhala Zofunika Kwambili

Anaona Nzelu Kukhala Zofunika Kwambili

Mfumukazi ya ku Sheba inayenda ulendo wautali komanso wovuta kuti ikaone Solomo (2 Mbiri 9:1, 2; w99 11/1 20 ¶4; w99 7/1 30 ¶4-5)

Itaona nzelu za Solomo na cuma cake, inasoŵa conena (2 Mbiri 9:3, 4; w99 7/1 30-31; onani cithunzi ca pacikuto)

Mfumukaziyo inatamanda Yehova cifukwa ca zimene inaona (2 Mbiri 9:7, 8; it-2 990-991)

Mfumukazi ya ku Sheba inaona kuti nzelu n’zofunika kwambili moti inalolela kutailapo zambili kuti izipeze.

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi nimayesetsa kufuna-funa nzelu mmene ningacitile pofuna-funa cuma cobisika?’—Miy. 2:1-6.