UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kufuna-funa Nzelu mwa Kuŵelenga Baibo Tsiku Lililonse
Nzelu zocokela kwa Mulungu n’zamtengo wapatali mofanana na cuma cobisika. (Miy. 2:1-6) Nzelu zimatithandiza kupanga zisankho zabwino, kukhala oganiza bwino, komanso zimatiteteza. Conco, nzelu “ni cinthu cofunika kwambili.” (Miy. 4:5-7) Kulimbikila n’kofunika kuti tipeze cuma cauzimu cobisika cimene cili m’Mawu a Mulungu. Tingayambe kucita izi mwa kumaŵelenga Mawu a Mulungu “usana ndi usiku,” kapena kuti tsiku lililonse. (Yos. 1:8) Onani zina zimene zingatithandize kuti tiziŵelenga Baibo nthawi zonse, komanso kuti tizisangalala poiŵelenga.
ONELELANI VIDIYO YAKUTI ACICEPELE PHUNZILANI KUKONDA MAWU A MULUNGU, KENAKO YANKHANI MAFUNSO AWA:
Ni zovuta zotani zimene acinyamatawa anakumana nazo pamene anali kuyesetsa kuŵelenga Baibo tsiku lililonse? Nanga n’ciyani cinawathandiza?
-
Melanie
-
Samuel
-
Celine
-
Raphaello
NDANDANDA YANGA YA KUŴELENGA BAIBO: