UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Mmene Tingagwilitsile Nchito Mavidiyo Okamba za Phunzilo la Baibo
Tili na mavidiyo anayi okamba za phunzilo la Baibo amene tingagwilitse nchito mu ulaliki. Kodi iliyonse mwa mavidiyo amenewa inapangidwa na colinga cotani?
-
N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibulo?—Yathunthu. Vidiyo imeneyi inakonzedwa pofuna kuthandiza anthu kukhala na cidwi cophunzila Baibo, mosasamala kanthu kuti amakhulupilila ciyani. Imalimbikitsa anthu kuphunzila Baibo kuti apeze mayankho pa mafunso ofunika kwambili mu umoyo. Ndipo imafotokozako mayankho ena ogwila mtima amene Baibo imapeleka. Imafotokozanso mmene munthu angapemphele phunzilo la Baibo.
-
N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibo? (yaifupi) Mfundo za m’vidiyo imeneyi ni zolingana na zimene zili mu vidiyo yathunthu, koma iyi ni yamphindi imodzi cabe. Ingakhale yothandiza kwambili m’magawo amene anthu amakhala otangwanika.
-
Kodi Phunzilo la Baibo Limacitika Bwanji? Vidiyo imeneyi inakonzedwa kuti izithandiza anthu kukhala na cifuno coyamba kuphunzila nafe Baibo kwaulele. Ndipo imayankha mafunso amene ambili amakhala nawo ponena za Phunzilo la Baibo, kuphatikizapo mmene angapemphele phunzilo.
-
Takulandilani ku Phunzilo Lanu la Baibo. Vidiyo imeneyi inakonzedwa kuti tiziionetsa kwa ophunzila Baibo. Ngakhale kuti vidiyoyi imachulidwa pa tsamba 2 m’buku lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!, tingaionetse pophunzila bulosha yakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! Vidiyoyi imafotokoza mwacidule zimene zili m’bukuli, komanso zimene wophunzila angayembekezele pophunzila.
Iliyonse mwa mavidiyo amenewa ili na colinga cake. Komabe, iliyonse tingaionetse kwa anthu kapena kuwatumizila pakakhala pofunikila. Ofalitsa akulimbikitsidwa kuwadziŵa bwino mavidiyo amenewa na kuwagwilitsa nchito mwaluso mu ulaliki.