Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Tate Apeleka Uphungu Wacikondi kwa Mwana Wake

Tate Apeleka Uphungu Wacikondi kwa Mwana Wake

Pa iwe wekha m’dziŵe bwino Yehova (1 Mbiri 28:9; w05 2/15 19 ¶9)

Tumikila Yehova na mtima wathunthu (1 Mbiri 28:9; w12 4/15 16 ¶13)

Dalila Yehova ndipo usacite mantha (1 Mbiri 28:20; w17.09 32 ¶20-21)

Mfumu Davide atakalamba, anapeleka malangizo amenewa kwa mwana wake wacinyamata komanso wosadziŵa zambili, Solomo, asanayambe kugwila nchito yofunika kwambili yomanga kacisi. N’cifukwa ciyani malangizo amenewa ni ofunika kwambili kwa tonsefe, maka-maka kwa Akhristu acinyamata?