March 20-26
2 MBIRI 1-4
Nyimbo 41 na Pemphelo
Mawu Oyamba (Mph. 1)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Mfumu Solomo Anapanga Cisankho Colakwika”: (Mph. 10)
Kufufuza Cuma Cauzimu: (Mph. 10)
2 Mbiri 1:11, 12—Kodi tiphunzilapo ciyani pa nkhaniyi za mapemphelo a munthu mwini? (w05 12/1 19 ¶6)
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, ni mfundo yopindulila iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (Mph. 4) 2 Mbiri 4:7-22 (th phunzilo 10)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Kuitanila Anthu ku Cikumbutso: (Mph. 3) Itanilani mnzanu wa kunchito, wa kusukulu, kapena wacibale. (th phunzilo 2)
Ulendo Wobwelelako: (Mph. 4) Citani ulendo wobwelelako kwa munthu amene analandila kapepala koitanila anthu ku Cikumbutso ndipo anaonetsa cidwi. M’fotokozeleni pulogilamu yathu yophunzila Baibo na anthu kwaulele, komanso m’gaŵileni bulosha yakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! Chulani na kukambilanako vidiyo yakuti Kodi Phunzilo la Baibulo Limacitika Bwanji? (Koma musaitambitse.) (th phunzilo 17)
Phunzilo la Baibo: (Mph. 5) lff phunzilo 09 mfundo 5 (th phunzilo 9)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kodi Mudzakhala Okonzeka pa Tsiku Lofunika Kwambili Caka Cino?: (Mph. 15) Nkhani komanso kutamba vidiyo. Ikambidwe na woyang’anila utumiki. Fotokozani mmene nchito yomemeza anthu ku Cikumbutso ikuyendela pampingo panu. Funsani mafunso ofalitsa amene anakumana na zocitika zolimbikitsa mu ulaliki. Chulankoni za ndandanda yoŵelenga Baibo pa nyengo ya Cikumbutso imene ili pa tsamba 8 na 9, ndipo limbikitsani onse kukonzekeletsa mitima yawo kaamba ka Cikumbutso. (Ezara 7:10) Fotokozani mmene tingawalandilile na manja aŵili alendo obwela ku Cikumbutso. (Aroma 15:7; mwb16.03 2) Onetsani vidiyo yakuti Mmene Mungapangile Mkate wa Cikumbutso.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (Mph. 30) lff phunzilo 41 mfundo 1-4
Mawu Othela (Mph. 3)
Nyimbo 135 na Pemphelo