Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Mfumu Solomo Anapanga Cisankho Colakwika

Mfumu Solomo Anapanga Cisankho Colakwika

[Onetsani vidiyo yakuti Mfundo Zokhudza Buku la 2 Mbiri.]

Solomo anasonkhanitsa mahosi na magaleta ambili ogulidwa ku Iguputo (Deut. 17:15, 16; 2 Mbiri 1:14, 17)

Mahosi na magaleta amenewo anali kugwilitsidwa nchito na gulu lankhondo la Solomo, ndipo panafunika mizinda yosungilako zinthu zimenezo komanso anthu ambili ozisamalila (2 Mbiri. 1:14; it-1 174 ¶5; 427)

Pa nthawi imene Solomo anali kulamulila bwino, Aisiraeli anali pa ulemelelo. Koma mu ulamulilo wa Mfumu Rehobowamu, iwo anapanduka cifukwa iye anapitiliza kuwasenzetsa goli lolemela la atate ake, komanso anawonjezela kulemela kwake. (2 Mbiri 10:3, 4, 14, 16) Zisankho zathu nthawi zonse zimakhala na zotulukapo zake.—Agal. 6:7.