March 27–April 2
2 MBIRI 5-7
Nyimbo 129 na Pemphelo
Mawu Oyamba (Mph. 1)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Kufufuza Cuma Cauzimu: (Mph. 10)
2 Mbiri 6:29, 30—Kodi mawu amenewa a m’pemphelo la Solomo angatilimbikitse bwanji? (w10 12/1 11 ¶7)
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, ni mfundo yopindulila iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (Mph. 4) 2 Mbiri 6:28-42 (th phunzilo 11)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Kuitanila Anthu ku Cikumbutso: (Mph. 3) Makambilano anu atsamile pa mfundo yaikulu ya makambilano acitsanzo. Mwininyumba akaonetsa cidwi, chulani na kukambilanako vidiyo yakuti Kukumbukila Imfa ya Yesu (koma musaitambitse.) (th phunzilo 3)
Ulendo Wobwelelako: (Mph. 4) Pambuyo pa nkhani ya Cikumbutso, yambitsani makambilano na munthu wacidwi amene wabwela. Ndipo yankhani funso limene wafunsa lokhudza mwambowo. (th phunzilo 17)
Nkhani: (Mph. 5) w93 2/1 31—Mutu: Tingacite Ciyani Ngati Sitinakwanitse Kupezeka pa Cikumbutso Cifukwa ca Vuto Linalake Lalikulu? (th phunzilo 18)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Uteteze Mtima Wako”: (Mph. 10) Kukambilana komanso kutamba vidiyo.
Zofunikila za Mpingo: (Mph. 5)
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (Mph. 30) lff phunzilo 41 mfundo 5, cidule cake, mafunso obweleza, komanso colinga
Mawu Othela (Mph. 3)
Nyimbo 34 na Pemphelo