CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Mtima Wanga Udzakhala Pamenepa Nthawi Zonse”
Yehova anadzisankhila yekha kacisi (2 Mbiri 7:11, 12)
Yehova anati nthawi zonse mtima wake udzakhala pa kacisiyo, kuonetsa kuti adzakhala na cidwi coona zimene zikucitika pa nyumbayo, imene inali kudziŵika na dzina lake (2 Mbiri 7:16; w02 11/15 5 ¶1)
Mulungu anati Aisiraeli akadzaleka kuyenda pamaso pake “ndi mtima wawo wonse,” iye adzalola kuti kacisiyo awonongedwe (2 Mbiri 6:14; 7:19-21; it-2 1077-1078)
Pa nthawi yopatulila kacisi, mwina anthuwo anali kuganiza kuti mitima yawo idzakhalabe pa kacisiyo nthawi zonse. Koma n’zacisoni kuti pang’ono-m’pang’ono, cangu cawo polambila Yehova cinacepa.
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi nimaonetsa bwanji kuti nimaika mtima wanga wonse pa kulambila?’