CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Kulambila pa Kacisi Kunayamba Kucitika Mwadongosolo Kwambili
Mfumu Davide anagaŵa Alevi na ansembe m’magulu-magulu kuti azigwila nchito za pakacisi (1 Mbiri 23:6, 27, 28; 24:1, 3; it-2 241, 686)
Akatswili oimba komanso anthu ena ophunzila kuimba anapatsidwa utumiki woimba nyimbo (1 Mbiri 25:1, 8; it-2 451-452)
Alevi anaikidwa kukhala alonda a pazipata, amsungacuma, komanso ogwila nchito zina (1 Mbiri 26:16-20; it-1 898)
Timalambila Yehova mwadongosolo cifukwa iye ni wadongosolo.—1 Akor. 14:33.
ZOYENELA KUZISINKHASINKHA: N’ciyani cionetsa kuti mpingo wacikhristu umacita zinthu mwadogosolo polambila Yehova masiku ano?