Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Mmene Tingathandizile Pakagwa Tsoka

Mmene Tingathandizile Pakagwa Tsoka

Matsoka a zacilengedwe akuculukila-culukila masiku ano. Tsoka likacitika, nchito yopeleka thandizo iyenela kucitika mwadongosolo komanso iyenela kuyang’anilidwa bwino. Pa cifukwa cimeneci, Bungwe Lolamulila linakonza zakuti pa ofesi ya nthambi iliyonse pakhazikitsidwe Dipatimenti Yoyang’anila Nchito Yopeleka Thandizo Pakagwa Tsoka.

Abale a m’dipatimenti imeneyi akamva kuti ku dela lina kwacitika tsoka la zacilengedwe, mwamsanga amakambilana na akulu a ku delalo kuti adziŵe thandizo limene angapeleke kwa ofalitsa. Ngati zimene zawonongeka n’zambili moti abale a m’delalo sangakwanitse kuthandizana okha-okha, ofesi ya nthambi imasankha abale oyenelela kuti atsogolele pa nchito yopeleka thandizo. Abalewo angapemphe anchito ongodzipeleka kapena angapemphe zinthu zina zofunikila, kapenanso angagule zinthu zofunikila ku dela lomwelo na kuzigaŵila kwa ofalitsa.

Kupeleka thandizo mwa njila imeneyi kuli bwino kusiyana n’kuti abale azingopeleka thandizo pa iwo okha. Kumathandiza kuti nchito imodzi isagwilike kaŵili, pasakhale msokonezo, komanso kuti tisawononge ndalama na zinthu zina zofunikila.

Abale oikidwa na ofesi ya nthambi amadziŵa kuculuka kwa ndalama zimene zikufunika, komanso kuculuka kwa anchito ongodzipeleka amene akufunika pa nchito yopeleka thandizo. Angadziŵanenso na akulu-akulu a m’delalo, amene nthawi zambili amathandiza kufulumizitsa nchito yopeleka thandizo. Conco, anthu sayenela kusonkhetsa ndalama, kutumiza thandizo ku dela limene kwagwa tsoka, kapena kupitako pokhapo ngati auzidwa kucita zimenezi.

Ngakhale n’conco, tsoka likacitika timafuna kupeleka thandizo. (Aheb. 13:16) Timawakonda abale athu! Nanga n’ciyani cimene tingacite? Koposa zonse, tingawapemphelele amene akumana na tsokalo, komanso amene akupeleka thandizo. Tingapelekenso thandizo mwa kucita copeleka ku nchito ya padziko lonse. Motsogoleledwa na Bungwe Lolamulila, maofesi a nthambi ndiwo amadziŵa bwino kumene ndalama zimenezi zingathandize kwambili. Ngati tifuna kukagwila nawo nchito yopeleka thandizo, tingaonetse kuti ndife okonzeka kuthandiza mwa kulemba fomu yakuti Local Design/Construction Volunteer Application (DC-50).

ONELELANI VIDIYO YAKUTI KUSEFUKILA KWA MADZI KOWONONGA KU BRAZIL, KENAKO YANKHANI FUNSO ILI:

N’ciyani cimakucititsani cidwi mukaganizila nchito yopeleka thandizo imene Mboni za Yehova zinagwila pamene madzi anasefukila ku Brazil mu 2020?