Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

April 22-28

MASALIMO 32-33

April 22-28

Nyimbo 103 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. N’cifukwa Ciyani Tiyenela Kuulula Macimo Akulu-akulu?

(Mph. 10)

Davide anapsinjika maganizo pamene anayesa kubisa macimo ake. Mwina linali chimo lokhudza Batiseba (Sal. 32:3, 4; w93 3/15 9 ¶7)

Davide anaulula chimo lake kwa Yehova ndipo anamukhululukila (Sal. 32:5; cl 262 ¶8)

Davide anakhala na mtendele wa mumtima Yehova atamukhululukila (Sal. 32:1; w01 6/1 30 ¶1)

Tikacita chimo lalikulu, modzicepetsa tiyenela kuulula na kuvomeleza zolakwa zathu kwa Yehova, na kum’pempha kuti atikhululukile. Tiyenelanso kupempha thandizo kwa akulu amene angatithandize kucila mwauzimu. (Yak. 5:14-16) Tikatelo Yehova adzatitsitsimula.—Mac. 3:19.

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 33:6—Kodi “mpweya wa m’kamwa” mwa Yehova n’ciyani? (w06 5/15 19 ¶13)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo ziti zothandiza zimene mungakonde kutigaŵilako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 33:1-22 (th phunzilo 11)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kudzicepetsa—Mmene Paulo Anaonetsela Khalidwe Limeneli

(Mph. 7) Kukambilana. Tambitsani VIDIYO, kenako kambilanani lmd phunzilo 4 mfundo 1-2.

5. Kudzicepetsa—Tengelani Citsanzo ca Paulo

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 74

6. Zofunikila za Mpingo

(Mph. 15)

7. Phunzilo la Baibo la Mpingo

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 39 na Pemphelo