Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

April 8-14

MASALIMO 26-28

April 8-14

Nyimbo 34 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Zimene Davide Anacita Kuti Asataye Cikhulupililo

(Mph. 10)

Davide anapempha Yehova kuti amuthandize kukhala na makhalidwe abwino (Sal. 26:1, 2; w04 12/1 14 ¶8-9)

Davide anapewa mayanjano oipa (Sal. 26:4, 5; w04 12/1 15 ¶12-13)

Davide anali kukonda kulambila Yehova (Sal. 26:8; w04 12/1 16 ¶17-18)


Ngakhale kuti Davide analakwitsapo zinthu zina, iye anakhalabe na “mtima wosagaŵanika.” (1 Maf. 9:4) Davide anali kukonda Yehova ndipo anam’tumikila na mtima wonse. Izi zinaonetsa kuti anali wokhulupilika.

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 27:10—Kodi lembali lingatilimbikitse bwanji mabwenzi athu a pamtima akatisiya? (w06 7/15 28 ¶15)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutigaŵilako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 27:1-14 (th phunzilo 2)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 2) KUNYUMBA NA NYUMBA. Seŵenzetsani thilakiti ya m’thuboksi yathu. (th phunzilo 3)

5. Kubwelelako

(Mph. 4) KUNYUMBA NA NYUMBA. Kambilanani funso ili kumbuyo kwa thilakiti imene munamusiyila ulendo wapita. Muuzeni za webusaiti ya jw.org, na kumuonetsako zinthu zina zimene zilipo. (lmd phunzilo 9 mfundo 3)

6. Nkhani

(Mph. 5) lmd zakumapeto A mfundo 3—Mutu: Zacilengedwe zimene zawonongedwa zidzakonzedwa n’kukhalanso zabwino-bwino. (th phunzilo 13)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 128

7. Acinyamata Amene Amakhalabe na Makhalidwe Abwino

(Mph. 15) Kukambilana.

Akhristu acinyamata ayenela kupewa makhalidwe aciwelewele. Iwo amalimbana na thupi lawo lopanda ungwilo ndipo amayesetsa kukhalabe oyela pamene ali pacimake pa unyamata. Iyi ni nthawi pamene cilakolako cakugonana cimakhala camphamvu. Ndipo izi zimacititsa kuti cikhale covuta kusunga makhalidwe abwino. (Aroma 7:21; 1 Akor. 7:36) Amalimbananso na cisonkhezelo cocokela kwa anzawo kuti acite zosayenela, monga kugonana na munthu asanaloŵe m’banja komanso zamathanyula. (Aef. 2:2) Timaŵanyadila acinyamata amene amasungabe cikhulupililo cawo.

Tambitsani VIDIYO yakuti Umoyo Wanga Nili Wacicepele—Kodi Ningakane Motani Ngati Nakakamizidwa Kugonana na Wina N’sanaloŵe M’banja? Kenako funsani omvela kuti:

  • Kodi Cory na Kamryn anali kusonkhezeledwa kucita ciyani?

  • N’ciyani cinaŵathandiza kusungabe cikhulupililo cawo?

  • Ni mfundo ziti za m’Baibo zingakuthandizeni zotelezi zikakucitikilani?

8. Phunzilo la Baibo la Mpingo

(Mph. 30) bt mutu 8 ¶5-12

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 38 na Pemphelo