Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

March 4-10

MASALIMO 16-17

March 4-10

Nyimbo 111 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Yehova Ndiye Gwelo la Ubwino

(Mph. 10)

Kukhala pa ubwenzi na atumiki a Yehova kumatibweletsela cimwemwe (Sal. 16:2, 3; w18.12 26 ¶11)

Kukhala pa ubwenzi wabwino na Yehova kumatikondweletsa ngako (Sal. 16:5, 6; w14 2/15 29 ¶4)

Citetezo ca Yehova cauzimu cimatipangitsa kukhala otetezeka (Sal. 16:8, 9; w08 2/15 3 ¶2-3)

Monga zinalili kwa Davide, ifenso timasangalala na umoyo cifukwa kutumikila Yehova amene ni gwelo la ubwino n’kofunika kwambili pa umoyo wathu.

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi umoyo wanga wasintha motani poyelekezela na mmene unalili n’sanaphunzile coonadi?’

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 17:8—Kodi mawu akuti “mwana wa diso” akunena za ciyani? (it-2 714)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutigaŵilako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 17:1-15 (th phunzilo 5)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 1) KUNYUMBA NA NYUMBA. Muitanileni ku Cikumbutso. (th phunzilo 11)

5. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) KUNYUMBA NA NYUMBA. Muitanileni ku Cikumbutso. Munthuyo akaonetsa cidwi, yelekezani kumutambitsa vidiyo yakuti, Kukumbukila Imfa ya Yesu, na kumuunikilako mfundo zake (th phunzilo 9)

6. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 2) ULALIKI WAMWAYI. Muitanileni ku Cikumbutso (th phunzilo 2)

7. Kupanga Ophunzila

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 20

8. Kodi Tingacikonzekele Bwanji Cikumbutso?

(Mph. 15) Kukambilana.

Pomvela lamulo la Yesu, tidzacita cikumbutso ca imfa yake pa Sondo, March 24. Tidzacita izi pokumbukila cikondi copambana cimene Yehova na Yesu anationetsa. (Luka 22:19; Yoh. 3:16; 15:13) Tingacikonzekele bwanji cocitika capadela cimeneci?

  • Tengan’koni mbali mokwanila pa kampeni yoitanila anthu ku nkhani yapadela komanso Cikumbutso. Lembani maina a anthu omwe mudzaitanila. Ngati ena sakhala m’dela lanu, fufuzani pa jw.org, kuti mupeze malo na nthawi ya misonkhano ya m’dela lawo

  • M’miyezi ya March na April, wonjezelani nthawi imene mumathela mu ulaliki. Kodi mungaciteko upainiya wothandiza wa maola 15 kapena 30?

  • Pa March 18, mukayambe kuŵelenga zocitika za mu mlungu wothela wa moyo wa Yesu pa dziko lapansi. Mungasankhe kuculuka kwa zimene muziŵelenga tsiku lililonse, potsatila “Ndandanda ya Kuŵelenga Baibo pa Nyengo ya Cikumbukutso ca 2024,” yomwe ili pa masamba 6-7

  • Pa tsiku la Cikumbutso, mukatambe pulogilamu yapadela ya Kulambila kwa M’maŵa pa jw.org

  • Pa Cikumbutso, mukaŵalandile na manja aŵili alendo komanso ozilala. Pambuyo pa Cikumbutso, mukapeze nthawi yoyankha mafunso omwe angadzakhale nawo. Konzani nthawi yoti mukawacezele pofuna kukulitsa cidwi cawo

  • Cikumbutso cikayandikila komanso pambuyo pake, sinkhasinkhani za dipo

Tambitsani VIDIYO yakuti Kukumbukila Imfa ya Yesu. Kenaka funsani omvela kuti:

Tingaiseŵenzetse bwanji vidiyo iyi pa kampeni yoitanila anthu ku Cikumbutso?

9. Phunzilo la Baibo la Mpingo

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 73 na Pemphelo