Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

March 3-9

MIYAMBO 3

March 3-9

Nyimbo 8 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Muzionetsa kuti Mumadalila Yehova

(Mph. 10)

Muzikhulupilila Yehova, m’malo modzidalila (Miy. 3:5; ijwbv nkhani 14 ¶4-5)

Onetsani kuti mumadalila Yehova mwa kufunafuna malangizo ake ndi kuwatsatila (Miy 3:6; ijwbv nkhani 14 ¶6-7)

Pewani kudalila luso lanu lomvetsa zinthu (Miy. 3:7; be-CN 76 ¶4)

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi nimafunafuna malangizo a Yehova m’zocita zanga zonse?’

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Miy. 3:3​—Kodi tingamange bwanji cikondi cokhulupilika komanso kukhulupilika m’khosi mwathu ndi kuzilemba pamtima pathu? (w06-CN 9/15 17 ¶7)

  • Pa kuwelenga Baibulo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuwelenga Baibulo

(Mph. 4) Miy. 3:​1-18 (th phunzilo 12)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Onetsani mmene mungayankhile munthu amene wakamba mawu ofala kwanuko ofuna kukanila ulaliki. (lmd phunzilo 1 mfundo 5)

5. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 4) ULALIKI WAPOYELA. Muuzeni za webusaiti ya jw.org ndi kumusiyila kakhadi koloŵela pa webusaiti imeneyi. (lmd phunzilo 3 mfundo 3)

6. Nkhani

(Mph. 5) w11-CN 3/15 14 7-10​—Mutu: Muzidalila Mulungu Mukakumana ndi Anthu Opanda Cidwi mu Ulaliki. (th phunzilo 20)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 124

7. Muzionetsa kuti Mumadalila Gulu la Yehova

(Mph. 15) Kukambilana.

N’cosavuta kukhulupilila Mawu a Mulungu ouzilidwa a coonadi ca m’Baibulo. Komabe, cimakhala covuta kutsatila malangizo ocokela kwa anthu opanda ungwilo amene amatsogolela gulu la Yehova, makamaka ngati sitinawamvetse malangizowo kapena kugwilizana nawo.

Welengani Malaki 2:7. Kenako funsani omvela kuti:

  • N’cifukwa ciyani n’zosadabwitsa kuti Yehova amagwilitsa nchito anthu opanda ungwilo kutsogolela anthu ake?

Welengani Mateyo 24:45. Kenako funsani omvela kuti:

  • N’cifukwa ciyani tiyenela kuwakhulupilila malangizo ocokela ku gulu la Yehova?

Welengani Aheberi 13:17. Kenako funsani omvela kuti:

  • N’cifukwa ciyani tiyenela kutsatila malangizo ocokela kwa anthu amene Yehova amawagwilitsa nchito kuti atitsogolele?

Tambitsani kambali ka VIDIYO YAKUTI Ciunikilo Na. 9 ca Bungwe Lolamulila mu 2021. Kenako funsani omvela kuti:

  • Kodi malangizo amene tinalandila pa nthawi ya mlili anakuthandizani bwanji kuti muzilikhulupilila kwambili gulu la Yehova?

8. Phunzilo la Baibulo la Mpingo

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 57 ndi Pemphelo