April 14-20
MIYAMBO 9
Nyimbo 56 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Khalani Munthu Wanzelu, Osati Wonyoza
(Mph. 10)
Munthu wonyoza amakana uphungu wacikondi, ndipo amakwiyila munthu yemwe wamupatsa uphunguwo (Miy. 9:7, 8a; w22.02 9 ¶4)
Munthu wanzelu amayamikila uphungu komanso yemwe wamupatsa uphunguwo (Miy. 9:8b, 9; w22.02 12 ¶12-14; w01-CN 5/15 30 ¶1-2)
Munthu wanzelu adzapeza mapindu, koma munthu wonyoza adzavutika (Miy. 9:12; w01-CN 5/15 30 ¶5)
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Miy. 9:17—Kodi “madzi akuba” n’ciyani? Nanga n’cifukwa ciyani “amatsekemela”? (w06-CN 9/15 17 ¶5)
Pa kuwelenga Baibulo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuwelenga Baibulo
(Mph. 4) Miy. 9:1-18 (th phunzilo 5)
4. Kubwelelako
(Mph. 4) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Munthuyo anapezeka ku Cikumbutso. (lmd phunzilo 8 mfundo 3)
5. Kubwelelako
(Mph. 4) ULALIKI WAPOYELA. Pa ulendo wapita, munathandiza munthuyo kupeza malo a kufupi ndi kwawo kumene kudzacitikila Cikumbutso. (lmd phunzilo 7 mfundo 4)
6. Kubwelelako
(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. Pa ulendo wapita, munathandiza wacibale wanu kupeza malo a kufupi ndi kwawo kumene kudzacitikila Cikumbutso. (lmd phunzilo 8 mfundo 4)
Nyimbo 84
7. Kodi Mwayi wa Utumiki Umakupangitsani Kukhala Apadela?
(Mph. 15) Kukambilana.
Tambitsani VIDIYO. Kenako funsani omvela kuti:
Kodi mawu akuti “utumiki” amatanthauza ciyani?
Kodi anthu amene ali ndi maudindo mumpingo ayenela kudziona bwanji?
N’cifukwa ciyani kutumikila ena n’kofunika kwambili kuposa kukhala ndi maudindo?
8. Phunzilo la Baibulo la Mpingo
(Mph. 30) bt mutu 25 ¶5-7, bokosi pa tsa. 200