April 28–May 4
MIYAMBO 11
Nyimbo 90 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Zimene Simuyenela Kukamba
(Mph. 10)
Pewani kukamba zinthu zimene zingakhumudwitse ‘anzanu’ (Miy. 11:9; w02-CN 5/15 26 ¶4)
Musamakambe zinthu zimene zingabweletse magawano (Miy. 11:11; w02-CN 5/15 27 ¶2-3)
Musamaulule nkhani zacinsinsi (Miy. 11:12, 13; w02-CN 5/15 27 ¶5)
ZOYENELA KUZISINKHASINKHA: Kodi mawu a Yesu a pa Luka 6:45 amatithandiza bwanji kupewa kukamba zinthu zoipa?
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
-
Miy. 11:17—Kodi timapindula bwanji tikamaonetsa ena kukoma mtima? (g20.1 11, bokosi)
-
Pa kuwelenga Baibulo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuwelenga Baibulo
(Mph. 4) Miy. 11:1-20 (th phunzilo 5)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. Pezani mpata wouzako munthu zimene munaphunzila pa msonkhano waposacedwa. (lmd phunzilo 2 mfundo 4)
5. Kubwelelako
(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. Gwilitsani nchito vidiyo ya m’thuboksi yathu. (lmd phunzilo 8 mfundo 3)
6. Kupanga Ophunzila
(Mph. 4) ULALIKI WAPOYELA. M’pempheni kuti muziphunzila naye Baibulo, ndipo muonetseni mmene phunzilo la Baibulo limacitikila. (lmd phunzilo 10 mfundo 3)
Nyimbo 157
7. Musalole Zokamba Zanu Kusokoneza Mtendele
(Mph. 15) Kukambilana.
Popeza ndife opanda ungwilo, nthawi zina timalakwitsa m’zokamba zathu. (Yak. 3:8) Koma tikamaganizila mavuto amene angabwele cifukwa cokamba zinthu zosayenela, tingapewe kukamba zinthu zimene tingadziimbe nazo mlandu pambuyo pake. Pansipa pali ena mwa makambidwe amene angasokoneze mtendele mumpingo:
-
Kudzitama. Kudzitama kumayambitsa kaduka ndi mpikisano.—Miy. 27:2
-
Kukamba mwacinyengo. Izi sizitanthauza kungokamba mabodza oonekelatu, koma ziphatikizapo kukamba zinthu mosaona mtima kuti usoceletse ena. Ngakhale mutakamba bodza limene lingaoneke laling’ono, anthu angasiye kukukhulupililani ndipo zingawononge mbili yanu.—Mlal. 10:1
-
Mijedo. Izi zitanthauza kukambilana zinthu zabodza zokhudza anthu ena, kapena kuulula nkhani zacinsinsi. (1 Tim. 5:13) Zimenezi zingabweletse kusamvana komanso magawano
-
Mawu aukali. Awa ndi mawu amene munthu amakamba mosadziletsa cifukwa cokwiya munthu wina akamukhumudwitsa. (Aef. 4:26) Mawu otelo angapweteke ena.—Miy. 29:22
Tambitsani VIDIYO YAKUTI Pewani Zinthu Zosokoneza Mtendele—Mbali Yake. Kenako funsani omvela kuti:
-
Kodi mwaphunzila ciyani za mmene mawu athu angasokonezele mtendele mumpingo?
Kuti muone mmene mtendele unabwezeletsedwela, onelelani vidiyo yakuti “Pezani Mtendele ndi Kuusunga.”
8. Phunzilo la Baibulo la Mpingo
(Mph. 30) bt mutu 25 ¶14-21