Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

April 7-13

MIYAMBO 8

April 7-13

Nyimbo 89 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Mvelani Yesu Amene Amachedwa Nzelu

(Mph. 10)

Yesu, amene amachedwa nzelu m’buku la Miyambo, ndiye anali “woyamba kulengedwa ndi Yehova” (Miy. 8:​1, 4, 22; cf-CN 131 ¶7)

Nzelu za Yesu komanso cikondi cake pa Atate wake zinakula panthawi yonse imene anakhala ndi Yehova polenga zinthu (Miy. 8:​30, 31; cf-CN 131-132 ¶8-9)

Timapindula ndi nzelu za Yesu tikamamumvela (Miy. 8:​32, 35; w09-CN 4/15 31 ¶14)

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Miy. 8:​1-3​—Kodi nzelu imangokhalila “kufuula mokweza” m’lingalilo lotani? (g-CN 5/14 16)

  • Pa kuwelenga Baibulo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuwelenga Baibulo

(Mph. 4) Miy. 8:​22-36 (th phunzilo 10)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kubwelelako

(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. Yankhani mafunso okhudza zimene zidzacitika pa Cikumbutso omwe munthu amene akufuna kukapezekapo angakhale nawo. (lmd phunzilo 9 mfundo 3)

5. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) ULALIKI WAMWAYI. Cikumbutso cisanayambe landilani munthu amene wabwela cifukwa anapeza kapepala kaciitano pakhomo pake. Pulogilamu ikatha yankhani mafunso amene angakhale nawo. (lmd phunzilo 3 mfundo 5)

6. Kufotokoza Zimene Mumakhulupilila

(Mph. 5) Nkhani. ijwbq nkhani 160​—Mutu: N’cifukwa Ciyani Baibulo Limati Yesu Ndi Mwana wa Mulungu? (th phunzilo 1)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 105

7. Zofunikila za Mpingo

(Mph. 15)

8. Phunzilo la Baibulo la Mpingo

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 7 ndi Pemphelo