March 24-30
MIYAMBO 6
Nyimbo 11 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Kodi Tingaphunzile Ciyani Kwa Nyelele?
(Mph. 10)
Tingatengepo maphunzilo ofunika kwambili tikaona mmene nyelele zimacitila zinthu (Miy. 6:6)
Ngakhale kuti zilibe wozitsogolela, mwacibadwa nyelele zimagwila nchito molimbika, zimagwilizana, ndipo zimakonzekelelatu zam’tsogolo (Miy. 6:7, 8; it-1-E 115 ¶1-2)
Pindulani mwa kutengela mmene nyelele zimacitila zinthu (Miy. 6:9-11; w00-CN 9/15 26 ¶3-4)
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
-
Miy. 6:16-19—Kodi mavesiwa akupeleka mndandanda wa zinthu zonse zimene Yehova amadana nazo? (w00-CN 9/15 27 ¶3)
-
Pa kuwelenga Baibulo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuwelenga Baibulo
(Mph. 4) Miy. 6:1-26 (th phunzilo 10)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. Itanilani wacibale wanu wozilala ku nkhani yapadela ndi Cikumbutso (lmd phunzilo 4 mfundo 3)
5. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. Pemphani abwana anu kuti akupatseni nthawi kuti mukapezekepo pa Cikumbutso. (lmd phunzilo 3 mfundo 3)
6. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. Itanilani munthuyo ku nkhani yapadela ndi Cikumbutso. (lmd phunzilo 5 mfundo 3)
Nyimbo 2
7. Cilengedwe Cimaonetsa Kuti Yehova Amafuna Kuti Tizikondwela—Nyama Zocititsa Cidwi
(Mph. 5) Kukambilana.
Tambitsani VIDIYO. Kenako funsani omvela kuti:
-
Kodi nyama zimatiphunzitsa ciyani za Yehova?
8. Zofunikila za Mpingo
(Mph. 10)
9. Phunzilo la Baibulo la Mpingo
(Mph. 30) bt mutu 24 ¶7-12, bokosi pa tsa. 193