Maulaliki Acitsanzo
NSANJA YA MLONDA
Funso: Kodi mukhulupilila kuti mau awa adzakwanilitsidwa?
Lemba: Chiv. 21:3, 4
Kugaŵila Cofalitsa: Nsanja ya Mlonda iyi ifotokoza mmene Mulungu adzakwanilitsila lonjezo limeneli ndi mmene mudzapindulila.
NSANJA YA MLONDA (tsamba lomaliza)
Funso: Ndifuna kukuonetsani funso ili. [Onetsani mwininyumba funso loyamba ndi mayankho amene ali patsamba 16 m’magazini iyi.] Kodi muganiza bwanji?
Lemba: Sal. 83:18
Kugaŵila Cofalitsa: Nkhani iyi ifotokoza zinthu zina zimene Baibulo limaphunzitsa zokhudza dzina la Mulungu
ZIMENE BAIBO IMAPHUNZITSA
Funso: Anthu ena amaganiza kuti Mulungu ndiye akulamulila dzikoli. Koma kodi mudziŵa kuti Baibulo siliphunzitsa zimenezo?
Lemba: 1 Yoh. 5:19
Kugaŵila Cofalitsa: Bukuli lifotokoza bwino zimene Baibulo limaphunzitsa m’ceniceni pa nkhani iyi komanso nkhani zina zambili.
LEMBANI ULALIKI WANU
Onani maulaliki acitsanzo amene asonyezedwa kale kuti akuthandizeni kulemba ulaliki wanu