May 16- 22
SALIMO 11-18
Nyimbo 106 ndi Pemphelo
Mau Oyamba (Mph. 3 kapena zocepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Ndani Amene Angakhale Mlendo m’Cihema ca Yehova?”: (Mph. 10)
Sal. 15:1, 2—Tifunika kulankhula zoona mumtima mwathu (w03-CN 8/1 14 ndime 18; w89-CN 9/15 26 ndime 7)
Sal. 15:3—Tiyenela kukamba zinthu zabwino (w89-CN 10/15 12 ndime 10-11; w89-CN 9/15 27 ndime 2-3; it-2 E 779)
Sal. 15:4, 5—Tiyenela kukhala okhulupilika m’zocita zathu (w06-CN 5/15 19 ndime 2; w89-CN 9/15 29-30; it-1 E 1211 ndime 3)
Kufufuza Cuma Cakuuzimu: (Mph. 8)
Sal. 11:3—Kodi vesili litanthauza ciani? (w06-CN 5/15 18 ndime 3; w05-CN 5/15 32 ndime 2)
Sal. 16:10—Kodi ulosi umenewu unakwanilitsidwa bwanji pa Yesu Kristu? (w11-CN 8/15 16 ndime 19; w05-CN 5/1 14 ndime 9)
Kodi kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno kwandiphunzitsa ciani za Yehova?
Ndi mfundo ziti pa kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ndingagwilitsile nchito mu ulaliki?
Kuŵelenga Baibulo: (Mph. 4 kapena zocepelapo) Salimo 18: 1- 19
KUONJEZELA LUSO LANU MU ULALIKI
Ulendo Woyamba: (Mph. 2 kapena zocepelapo) Nsanja ya Mlonda ya 2016 Na. 3 tsa. 16—Ŵelengani lemba pa foni kapena pa tabuleti.
Ulendo Wobwelelako: (Mph. 4 kapena zocepelapo) Nsanja ya Mlonda ya 2016 Na. 3 tsa. 16—Ŵelengani malemba pa JW Laibulale kuti mwininyumba aone mmene alembedwela m’cinenelo cake. Ngati mulibe foni kapena tabuleti, pemphani mwininyumba kuti aŵelenge m’Baibulo lake.
Phunzilo la Baibulo: (Mph. 6 kapena zocepelapo) bh 100-101 ndime 10-11—Mwacidule wofalitsa aonetse wophunzila mmene angaseŵenzetsele JW Laibulale kuti apeze yankho la funso lake. Ngati mulibe foni kapena tabuleti, seŵenzetsani Buku Lofufuzila Nkhani kapena Watchtower Publications Index, kuti mupeze yankho la funso limene wafunsa.
UMOYO WATHU WACIKRISTU
“Mmene Tingaseŵenzetsele JW Laibulale”—Mbali 1: (Mph. 15) Kukambilana. Onetsani mavidiyo akuti Set and Manage Bookmarks ndi Use History, ndipo kambilanani mwacidule mavidiyo amenewa ngati alipo. Ndiyeno, kambilanani tumitu tuŵili pa nkhani imene mukukambilana. Pemphani omvela kuti akambe njila zina za mmene anagwilitsila nchito JW Laibulale pocita phunzilo laumwini ndi pamisonkhano yampingo.
Phunzilo la Baibulo la Mpingo: (Mph. 30) ia mutu 15 ndime 15-26, ndi kubwelelamo pa tsa. 134
Kubweleza Mfundo Zimene Taphunzila ndi Kufotokoza Zomwe Tidzaphunzila Mlungu Wotsatila (Mph. 3)
Nyimbo 43 ndi Pemphelo