SALIMO 11-18
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU |Ndani Amene Angakhale Mlendo m’Cihema ca Yehova?
Kuti munthu akhale mlendo m’cihema ca Yehova afunika kukhala bwenzi la Mulungu, kumukhulupilila ndi kumumvela. Lemba la Salimo 15 limafotokoza zimene Yehova amafuna mwa bwenzi lake.
MLENDO WA YEHOVA AYENELA . . .
-
kukhala wokhulupilika
-
kulankhula zoona mumtima mwake
-
kulemekeza atumiki a Yehova
-
kusunga mau ake zivute zitani
-
kuthandiza osoŵa popanda kuyembekezela kuti naonso adzamuthandiza
MLENDO WA YEHOVA AMAPEWA . . .
-
misece ndi kunama
-
kucitila mnzake zoipa
-
kudyela masuku pamutu Akristu anzake
-
kugwilizana ndi anthu amene satumikila Yehova
-
kulandila ciphuphu