Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

May 2-8

YOBU 38-42

May 2-8
  • Nyimbo 63 ndi Pemphelo

  • Mau Oyamba (Mph. 3 kapena zocepelapo)

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

  • Yehova Amakondwela Tikamapemphelela Ena”: (Mph. 10)

    • Yobu 42:7, 8—Yehova anafuna kuti Yobu apemphelele Elifazi, Bilidadi ndi Zofari (w13-CN 6/15 21 ndime 17; w98-CN 5/1 30 ndime 3-6)

    • Yobu 42:10—Yehova anacilitsa Yobu atapemphelela anzake atatu aja (w98-CN 5/1 31 ndime 3)

    • Yobu 42:10-17—Yehova anadalitsa Yobu kwambili cifukwa ca cikhulupilililo cake ndi kupilila kwake (w94-CN 11/15 20 ndime 19-20)

  • Kufufuza Cuma Cakuuzimu (Mph. 8)

    • Yobu 38:4-7—Kodi “nyenyezi za m’maŵa” ndani? Nanga timadziŵa ciani za io? (bh 97 ndime 3)

    • Yobu 42:3-5—N’ciani cingatithandize kuona Mulungu monga mmene Yobu anali kumuonela? (w15-CIN 10/15 8 ndime 16-17)

    • Kodi kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno kwandiphunzitsa ciani za Yehova?

    • Ndi mfundo ziti pa kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ndingagwilitsile nchito mu ulaliki?

  • Kuŵelenga Baibulo: (Mph. 4 kapena zocepelapo) Yobu 41: 1- 26

KUONJEZELA LUSO LANU MU ULALIKI

  • Konzekelani Maulaliki a Mwezi Uno: (Mph. 15) Kukambilana. Onetsani mavidiyo a maulaliki acitsanzo ndi kukambilana mfundo zake. Mwacidule fotokozani mfundo za m’nkhani yakuti “Mmene Tingaseŵenzetsele JW Laibulale,” pokambilana mmene tingagwilitsile nchito foni kapena tabuleti. Kumbutsani ofalitsa kuti mwezi uliwonse azipeleka lipoti la ciŵelengelo ca nthawi imene atambitsa vidiyo mu ulaliki. Limbikitsani ofalitsa kulemba ulaliki wao.

UMOYO WATHU WACIKRISTU

  • Nyimbo 60

  • Kodi Mukugwilitsila Nchito JW Laibulale?”: (Mph. 15) Coyamba, kambilanani nkhani imeneyi kwa mphindi 5. Ndiyeno, onelelani ndi kukambilana vidiyo yakuti, Yambani Kugwilitsila Nchito “JW Laibulale.” Pambuyo pake, muonelelenso vidiyo yofotokoza za kucita daunilodi, kusunga, ndi kuŵelenga zofalitsa. (Download and Manage Publications ndi Customize the Reading Experience). Ngati mavidiyo amenewa palibe, kambilanani nkhani yakuti “Webu Saiti Yathu—Igwilitsileni Nchito Polalikila” imene ili mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa December 2012. Limbikitsani onse amene angathe kuti aike JW Laibulale pa zipangizo zao zokhala ndi intaneti, ndi kucita daunilodi zofalitsa. Angacite zimenezi mlungu wa May 16 usanafike, pamene tidzaphunzila nkhani yakuti “Mmene Tingaseŵenzetsele JW Laibulale.”

  • Phunzilo la Baibulo la Mpingo: (Mph. 30) ia mutu 14 ndime 14-22, ndi kubwelelamo pa tsa. 124

  • Kubweleza Mfundo Zimene Taphunzila ndi Kufotokoza Zomwe Tidzaphunzila Mlungu Wotsatila (Mph. 3)

  • Nyimbo 77 ndi Pemphelo