May 9- 15
SALIMO 1-10
Nyimbo 99 ndi Pemphelo
Mau Oyamba (Mph. 3 kapena zocepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Kuti Tikhale Pamtendele ndi Mulungu, Tifunika Kulemekeza Mwana Wake, Yesu”: (Mph. 10)
[Onetsani Vidiyo Yofotokoza Buku la Masalimo]
Sal. 2:1-3—Ulosi unakambilatu kuti anthu adzatsutsa ulamulilo wa Yehova ndi Yesu (w04-CN 7/15 16-17 ndime 4-8; it-1 E 507; it-2 E 386 ndime 3)
Sal. 2:8-12—Anthu amene amalemekeza Mfumu yodzozedwa ndi Yehova, ndi okhawo amene adzalandila moyo (w04-CN 8/1 5 ndime 2-3)
Kufufuza Cuma Cakuuzimu (Mph. 8)
Sal. 2:7—Kodi “lamulo la Yehova” n’ciani? (w06-CN 5/15 17 ndime 6)
Sal. 3:2—Kodi liu lakuti Selah limatanthauza ciani? (Onani mau amunsi pa Salimo 3:2 mu Baibulo la Dziko Latsopano)
Kodi kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno kundiphunzitsa ciani za Yehova?
Ndi mfundo ziti pa kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ndingagwilitsile nchito mu ulaliki?
Kuŵelenga Baibulo: (Mph. 4 kapena zocepelapo) Salimo 8:1–9:10
KUONJEZELA LUSO LANU MU ULALIKI
Ulendo Woyamba: (Mph. 2 kapena zocepelapo) Nsanja ya Mlonda ya 2016 Na. 3 nkhani ya pacikuto—Ŵelengani lemba pa foni yanu kapena pa tabuleti.
Ulendo Wobwelelako: (Mph. 4 kapena zocepelapo) Nsanja ya Mlonda ya 2016 Na. 3 nkhani ya pacikuto—Citani citsanzo coonetsa mwininyumba akukana kuti wofalitsa amuŵelengele lemba poseŵenzetsa Baibulo la Dziko Latsopano. Ndiyeno, wofalitsayo aseŵenzetse JW Laibulale kuti amuonetse mmene lembalo analimasulila m’Baibulo lina. Ngati n’zosatheka kuseŵenzetsa JW Laibulale, pemphani mwininyumba kuti aŵelenge lembalo m’Baibulo lake.
Phunzilo la Baibulo: (Mph. 6 kapena zocepelapo) bh 12 ndime 12-13—Limbikitsani wophunzila Baibulo kuti acite daunilodi JW Laibulale pa foni kapena pa tabuleti yake.
UMOYO WATHU WACIKRISTU
Muzilemekeza Nyumba ya Yehova: (Mph. 5) Kukambilana. Tambitsani vidiyo ya pa jw.org yakuti Khala Bwenzi la Yehova—Muzilemekeza Nyumba ya Yehova. (Pitani pa ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ANA.) Ngati palibe vidiyo, mungakambilane cithunzi cimene cili patsamba 29 mu Nsanja ya Mlonda ya July 15, 2015. Kenako, pemphani ana kubwela kupulatifomu kuti muwafunse mafunso okhudza vidiyo imeneyi.
Dzina la Mulungu m’Malemba Aciheberi: (Mph. 10) Nkhani yocokela mu Buku Lothandiza Pophunzila Mau a Mulungu, cigawo 1.
Phunzilo la Baibulo la Mpingo: (Mph. 30) ia mutu 15 ndime 1-14, ndi bokosi pa tsa. 138
Kubweleza Mfundo Zimene Taphunzila ndi Kufotokoza Zomwe Tidzaphunzila Mlungu Wotsatila (Mph. 3)
Nyimbo 11 ndi Pemphelo