May 14-20
MALIKO 9-10
Nyimbo 22 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 min. olo kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Masomphenya Olimbitsa Cikhulupililo”: (10 min.)
Maliko 9:1—Yesu analonjeza kuti ena mwa atumwi ake adzaona masomphenya a ulemelelo umene iye adzakhala nawo mu Ufumu (w05 1/15 peji 12 pala. 9-10)
Maliko 9:2-6—Petulo, Yakobo, na Yohane anaona Yesu atasandulika, ndipo anali kukambilana na “Eliya” na “Mose” (w05 1/15 peji 12 pala. 11)
Maliko 9:7—Yehova iye mwini anakamba motsimikiza kuti Yesu ni Mwana wake (“mau” nwtsty mfundo younikila)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Maliko 10:6-9—Ni mfundo iti yokhudza cikwati imene Yesu anaunika? (w08 2/15 peji 30 pala. 8)
Maliko 10:17, 18—N’cifukwa ciani Yesu anawongolela munthu wina cifukwa comutomola kuti “Mphunzitsi Wabwino”? (“Mphunzitsi Wabwino,” “Palibe wabwino, koma Mulungu yekha” nwtsty mfundo zounikila)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Maliko 9:1-13
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (2 min. olo kucepelapo) Seŵenzetsani makambilano acitsanzo.
Vidiyo ya Kubwelelako Koyamba: (5 min.) Tambitsani na kukambilana vidiyoyi.
Nkhani: (6 min. olo kucepelapo) w04 5/15 mape. 30-31—Mutu: Kodi Mau a Yesu Opezeka pa Maliko 10:25 Atanthauzanji?
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Cimene Mulungu Wacimanga Pamodzi . . . ”: (15 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyo yakuti Cikondi na Ulemu Zimagwilizanitsa Banja.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu. 20
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 66 na Pemphelo