Masomphenya Olimbitsa Cikhulupililo
Ganizilani mmene Yesu anamvelela m’masomphenya a kusandulika kwake, pamene Atate ake akumwamba analengeza kuti amakondwela naye. Mosakayikila, izi zinalimbikitsa Yesu kuti apilile mavuto amene anali kudzakumana nawo. Masomphenyawa analimbitsanso kwambili cikhulupililo ca Petulo, Yakobo, na Yohane. Anawatsimikizila kuti Yesu analidi Mesiya, ndi kuti iwo anacita bwino kumumvetsela. Ngakhale pambuyo pa zaka 32, Petulo anali kukumbukilabe cocitikaci na mmene cinalimbitsila cikhulupililo cake mu “mau aulosi.”—2 Pet. 1:16-19.
Olo kuti ise sitinaoneko masomphenya ocititsa cidwi amenewo, tikuona kukwanilitsidwa kwake. Yesu lomba akulamulila monga Mfumu ya mphamvu. Posacedwapa, ‘adzapambana pa nkhondo yolimbana’ na adani ake, kuti pakhale dziko latsopano lolungama.—Chiv. 6:2.
Kodi cikhulupililo canu calimba bwanji poona kukwanilitsika kwa ulosi wa m’Baibo umenewu?