May 21-27
MALIKO 11-12
Nyimbo 34 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 min. olo kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Mkaziyo Anaponya Zambili Kuposa Ena Onse”: (10 min.)
Maliko 12:41, 42—Yesu anaona mkazi wamasiye wosauka akuponya tundalama tuŵili tocepa mphamvu m’coponyamo zopeleka pa kacisi (“moponyamo zopeleka”, “timakobidi tiŵili tating’ono” nwtsty mfundo zounikila)
Maliko 12:43—Yesu anayamikila copeleka ca mkaziyo, ndipo anachula zimenezi kwa ophunzila ake (w97 10/15 mape. 16-17 mapa. 16-17)
Maliko 12:44—Copeleka ca mkazi wamasiye cinali ca mtengo wapatali kwa Yehova (w97 10/15 peji 17 pala. 17; w87 12/1 peji 29 pala. 7; cl peji 185 pala. 15)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Maliko 11:17—N’cifukwa ciani Yesu anachula kacisi kuti “nyumba yopemphelelamo mitundu yonse”? (“nyumba yopemphelelamo mitundu yonse” nwtsty mfundo younikila)
Maliko 11:27, 28—Kodi “zinthu” zimene otsutsa Yesu anali kukamba zinali ciani? (jy peji 244 pala. 7)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Maliko 12:13-27
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (2 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo. Mwininyumba akambe zimene anthu a m’gawo lanu amakonda kukamba pokana kuwalalikila.
Kubwelelako Koyamba: (3 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo. Mwininyumba akukuuzani kuti m’bululu wake anamwalila posacedwa.
Vidiyo ya Kubwelelako Kaciŵili: (5 min.) Tambitsani na kukambilana vidiyoyi.