UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Yehova Adzakuthandiza Kukhala Wolimba Mtima
Ngati mumayenda ku sukulu, kodi mumayopa kulalikila na kuuza ena kuti ndimwe wa Mboni za Yehova? Ngati n’conco, mungacite ciani kuti mukhale ‘wolimba mtima’ polalikila za Yehova? (1 Ates. 2:2) Kodi imwe muli na zifukwa zanji zokhalila wolimba mtima? Pambuyo potamba vidiyo ya mutu wakuti Yehova Adzakuthandiza Kukhala Wolimba Mtima, yankhani mafunso otsatilawa:
-
Ni citsanzo citi ca m’Baibo cimene cinathandiza Sofiya kukhala wolimba mtima?
-
Kodi Sofiya anapindula bwanji cifukwa coyesezelatu mmene angalalikilile?
-
N’cifukwa ciani mufunika kuwalalikila anzanu a kusukulu?
-
Ngati simuli pa sukulu, kodi vidiyo imeneyi yakuthandizani bwanji?