Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Onetsani Cikondi m’Banja

Onetsani Cikondi m’Banja

Cikondi cili ngati guluu. Cimagwilizanitsa banja. Popanda cikondi, m’banja simungakhale mgwilizano. Kodi amuna, akazi, na makolo angaonetse bwanji cikondi m’banja?

Mwamuna wacikondi amaganizila zosoŵa za mkazi wake, maganizo ake, komanso mmene amamvelela. (Aef. 5:28, 29) Amasamalila banja lake kuthupi na kuuzimu kuphatikizapo kucititsa Kulambila kwa Pabanja nthawi zonse. (1 Tim. 5:8) Mkazi wacikondi amagonjela mwamuna wake na ‘kumulemekeza kwambili.’ (Aef. 5:22, 33; 1 Pet. 3:1-6) Mwamuna na mkazi wake, ayenela kukhala okonzeka kukhululukilana na mtima wonse. (Aef. 4:32) Makolo acikondi amaonetsa cidwi kwa mwana aliyense, ndiponso amaphunzitsa ana awo kukonda Yehova. (Deut. 6:6, 7; Aef. 6:4) Amadzifunsa kuti, ‘Kodi ana athu amakumana na mavuto otani kusukulu? Kodi amacita bwanji ngati anzawo awanyengelela kucita zolakwika?’ Ngati m’banja muli cikondi, onse amadziona kuti ni otetezeka.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI ONETSANI CIKONDI COSATHA M’BANJA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Kodi mwamuna wacikondi amadyetsa bwanji mkazi wake kuuzimu na kuthupi komanso kumuonetsa cikondi?

  • Kodi mkazi wacikondi amaonetsa bwanji kuti amam’lemekeza kwambili mwamuna wake?

  • Kodi makolo acikondi amakhomeleza bwanji Mawu a Mulungu mwa ana awo?