Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Muzipanga Zosankha Mwanzelu pa Nkhani ya Moŵa

Muzipanga Zosankha Mwanzelu pa Nkhani ya Moŵa

Akhristu onse ayenela kudziletsa pankhani ya kumwa zakumwa zoledzeletsa. (Miy. 23:20, 29-35; 1 Akor. 6:9, 10) Ngati Mkhristu wasankha kumwako moŵa, ayenela kucita zimenezo mwacikatikati. Ayenelanso kupewa kudalila moŵa pocita zinthu. Komanso, ayenela kupewa kukhumudwitsa ena. (1 Akor. 10:23, 24; 1 Tim. 5:23) Conco, tiyenela kupewa kukakamiza aliyense kumwa moŵa, maka-maka acinyamata.

ONETSANI VIDIYO YA ZITHUNZI ZOJAMBULA PAMANJA YAKUTI GANIZILANI ZOTULUKAPO ZA KUMWA MOŴA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO AWA:

  • N’cifukwa ciani Akhristu onse ayenela kutsatila malamulo a boma okhudza kumwa moŵa?—Aroma 13:1-4

  • N’cifukwa ciani sitiyenela kulola ena kutikakamiza kumwa moŵa?—Aroma 6:16

  • Pankhani ya moŵa, kodi mungapewe bwanji zocitika zimene zingakugwetseleni m’mavuto?