CITANI KHAMA PA ULALIKI | WONJEZELANI CIMWEMWE CANU MU ULALIKI
Kambani Mwaumoyo Pophunzitsa
Anthu amakhudzidwa ngati tikamba mwaumoyo. Kukamba mwaumoyo kumasonkhezela anthu kumvetsela zimene tikamba. Kumaonetsanso kuti timaona uthenga wathu kukhala wofunika. Tingakwanitse kukamba mwaumoyo mosasamala kanthu za cikhalidwe cathu kapena cibadwa cathu. (Aroma 12:11) Motani?
Coyamba, ganizilani za kufunika kwa uthenga wanu. Muli na mwayi ‘wolengeza uthenga wabwino wa zinthu zabwino.’ (Aroma 10:15) Caciŵili, ganizilani mmene uthenga wabwino udzapindulitsila omvela anu. Uthenga wanu ni wofunika kwambili kwa iwo. (Aroma 10:13, 14) Cotsiliza, kambani mwaumoyo, pangani magesica mwacibadwa, ndipo khope yanu izionetsa mmene mumvelela.
ONELELANI VIDIYO YAKUTI PEZANI CIMWEMWE PA NCHITO YOPANGA OPHUNZILA—NOLANI MALUSO ANU—KUKAMBA MWAUMOYO POPHUNZITSA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO AYA:
-
N’ciani cinacititsa kuti cidwi ca Neeta cotsogoza phunzilo la Baibo kwa Rose cicepe?
-
N’ciani cinapangitsa kuti Neeta akhalenso na cidwi cotsogoza phunzilo kwa Rose?
-
N’cifukwa ciani tiyenela kusumika maganizo athu pa makhalidwe abwino a omvela athu?
-
Kodi kukamba mwaumoyo kungakhudze bwanji ophunzila Baibo athu na ena?