Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CITANI KHAMA PA ULALIKI | WONJEZELANI CIMWEMWE CANU MU ULALIKI

Seŵenzetsani Mafanizo Pofotokoza Mfundo Zazikulu

Seŵenzetsani Mafanizo Pofotokoza Mfundo Zazikulu

Popanga maulendo obwelelako kapena potsogoza maphunzilo a Baibo, tifunika kuthandiza omvela athu kumvetsetsa mfundo zazikulu. Tingacite bwanji zimenezi? Tiyenela kuseŵenzetsa mafanizo. Tikatelo, tidzawafika pamtima omvela, komanso tidzawathandiza kumakumbukila mfundo zimene tawaphunzitsa.

Pamene mukonzekela ulendo wobwelelako kapena kukatsogoza phunzilo la Baibo, onani mfundo zazikulu zimene mufuna kukafotokoza poseŵenzetsa mafanizo, osati mfundo zing’ono-zing’ono. Ndiyeno pezani mafanizo osavuta kumva ozikidwa pa zocitika za tsiku na tsiku. (Mat. 5:14-16; Maliko 2:21; Luka 14:7-11) Muyenelanso kuganizila cikhalidwe na zocitika za pa umoyo wa womvela wanu. (Luka 5:2-11; Yoh. 4:7-15) Mudzapeza cimwemwe poona kuti womvela wanu akukondwela na mfundo imene mwamuthandiza kumvetsetsa.

ONETSANI VIDIYO YAKUTI PEZANI CIMWEMWE PA NCHITO YOPANGA OPHUNZILA—NOLANI MALUSO ANU—KUSEŴENZETSA MAFANIZO POFOTOKOZA MFUNDO ZOFUNIKA KWAMBILI, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • N’cifukwa ciani ophunzila Baibo amafunika kuwathandiza kuti amvetsetse mavesi a m’Baibo?

  • Kodi mlongo Neeta waseŵenzetsa bwanji fanizo pofotokoza mfundo ya coonadi ya pa Aroma 5:12?

  • Mafanizo abwino amawafika pamtima omvetsela

    Kodi mafanizo abwino angawakhudze bwanji omvela athu?

  • N’cifukwa ciani mu ulaliki tiyenela kuseŵenzetsa mavidiyo na zida zina zophunzitsila zimene gulu la Yehova latipatsa?