Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Cilango Cimaonetsa Cikondi ca Yehova

Cilango Cimaonetsa Cikondi ca Yehova

Cilango nthawi zambili cimatanthauza kupeleka malangizo na kuphunzitsa. Koma cingaphatikizeponso uphungu na cibalo kapena kuti mkwapulo. Yehova amatilanga n’colinga cakuti tizimulambila m’njila yovomelezeka. (Aroma 12:1; Aheb. 12:10, 11) Nthawi zina cilango cimakhala cowawa, koma cimabala cilungamo na kubweletsa madalitso. (Miy. 10:7) Kodi wopeleka cilango na wocilandila ayenela kukumbukila ciani?

Wopeleka cilango. Akulu, makolo, na ena amayesetsa kupeleka cilango mokoma mtima komanso mwacikondi monga mmene Yehova amacitila. (Yer. 46:28) Ngakhale uphungu wamphamvu uyenela kupelekedwa mogwilizana na mmene mikhalidwe ilili, ndiponso mosonkhezeledwa na cikondi.—Tito 1:13.

Wolandila cilango. Kaya cilango capelekedwa motani, sitiyenela kucikana koma tiyenela kugwililapo nchito mwamsanga. (Miy. 3:11, 12) Monga anthu opanda ungwilo tonsefe timafunikila cilango. Cilango cimabwela m’njila zosiyana-siyana. Tingacilandile kupitila m’zimene timaŵelenga m’Baibo kapena zimene timamvetsela pa misonkhano ya mpingo. Nthawi zina ena amafunikila cilango ca komiti ya ciweluzo. Ngati tilandila cilango na kucitapo kanthu, tidzakhala na umoyo wabwino komanso tidzapeza moyo wosatha.—Miy. 10:17.

ONETSANI VIDIYO YAKUTI “YEHOVA AMALANGA ALIYENSE AMENE IYE AMAMUKONDA,” NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Kodi umoyo wa m’bale Canon unali bwanji poyamba? Nanga unasintha bwanji?

  • Ni cilango cotani cacikondi cimene analandila kucokela kwa Yehova?

  • Phunzilani kukonda cilango ca Yehova

    Taphunzilapo ciani pa citsanzo cake?