May 3-9
NUMERI 27–29
Nyimbo 106 na Pemphelo
Mawu Oyamba (Mph. 1)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Tengelani Citsanzo ca Yehova ca Kupanda Tsankho”: (Mph. 10)
Kufufuza Cuma Cauzimu: (Mph. 10)
Num. 28:7, 14—Kodi nsembe zacakumwa zinali zotani? (1 Sam. 1:11; it-2 528 ¶5)
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (Mph. 4) Num. 28:11-31 (th phunzilo 5)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (Mph. 5) Kukambilana. Onetsani vidiyo yakuti Ulendo Woyamba: Colinga ca Mulungu—Gen. 1:28. Nthawi iliyonse vidiyo ikaima, na imwe iimitseni na kufunsa omvetsela mafunso amene aonekela pasikilini.
Ulendo Woyamba: (Mph. 3) Seŵenzetsani makambilano acitsanzo. (th phunzilo 4)
Nkhani: (Mph. 5) w07 4/1 17-18—Mutu: N’ciani Cimapangitsa Nsembe Kukhala Zovomelezeka kwa Yehova? (th phunzilo 16)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Khala Bwenzi la Yehova—Uzikonda Mnzako: (Mph. 6) Kukambilana. Onetsani vidiyoyi. Ndiyeno ngati n’kotheka, funsani ana amene munawakonzekeletsa mafunso aya: N’cifukwa ciani ana a sukulu anali kumusala Priya? Kodi Sophia anamuonetsa bwanji cikondi Priya? Kodi mungawaonetse bwanji cikondi anthu a cikhalidwe cina?
Kodi Bwenzi Leni-leni Limakhala Lotani?: (Mph. 9) Kukambilana. Onetsani vidiyoyi ya zithunzi zojambula pamanja. Ndiyeno funsani omvetsela mafunso aya: Kodi muyenela kusankha munthu wotani kuti akhale bwenzi lanu? Kodi bwenzi labwino mungalipeze kuti? Mungacite ciani kuti mupange ubwenzi wabwino na ena?
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (Mph. 30) lfb phunzilo 35
Mawu Othela (Mph. 3)
Nyimbo 41 na Pemphelo