Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Khalanibe Wokonzeka m’Ndime Ino Yothela ya “Masiku Otsiliza”

Khalanibe Wokonzeka m’Ndime Ino Yothela ya “Masiku Otsiliza”

Popeza tikhala m’ndime yothela ya masiku otsiliza, tiyembekezela kukumana na mavuto aakulu. (2 Tim. 3:1; mfundo younikila pa Mat. 24:8) Tsoka la zacilengedwe likacitika, anthu a Yehova nthawi zambili amalandila malangizo a panthawi yake opulumutsa moyo. Kuti tikapulumuke panthawiyo, tiyenela kukhala omvela ndiponso kukonzekela pali pano kuuzimu na kuthupi.—Luka 16:10.

  • Konzekelani kuuzimu: Khalani na cizoloŵezi cabwino cocita zinthu zauzimu. Phunzilani kucita maulaliki osiyana-siyana. Musataye mtima ngati kwakanthawi mwapezeka kuti muli kwanokha kopanda abale na alongo anu auzimu. (Yes. 30:15) Kumbukilani kuti Yehova na Yesu amakhala nanu nthawi zonse.—od 176 ¶15-17

  • Konzekelani kuthupi: Banja lililonse liyenela kukhala na cola cokhala na zinthu zofunikila pakagwa tsoka. Liyenelanso kusungako cakudya cokwanila, madzi, mankhwala, na zinthu zina zaconco, zimene angagwilitsile nchito ngati angafunikile kukhala panyumba kapena ku malo ena otetezeka kwa nthawi yotalikilapo.—Miy. 22:3; g17.5 4, 6

ONELELANI VIDIYO YAKUTI KODI MWAKONZEKELA TSOKA LA ZACILENGEDWE? NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Kodi mungakonzekele bwanji kuuzimu tsoka la zacilengedwe lisanacitike?

  • N’cifukwa ciani tiyenela . . .

    • kumakambilana na akulu nthawi na nthawi?

    • kukhalilatu na cola ca zofunikila pakacitika tsoka la zacilengedwe?

    • kukambilana mitundu ya masoka a zacilengedwe amene angacitike komanso zimene tingacite pa tsoka lililonse?

  • Ni zinthu zitatu ziti zimene tingacite pothandiza anthu amene akhudzidwa na tsoka linalake?

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi mlili wa COVID-19 waniphunzitsa ciani pa nkhani yokonzekela masoka a zacilengedwe?’