UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Muzilamulila Zilakolako Zanu
Pokhala anthu opanda ungwilo, nthawi zonse timafunika kucita kulimbikila kulamulila zilakolako zathu. Popanda kucita zimenezi, tingataye ciyanjo ca Yehova. Mwacitsanzo, ena pofunitsitsa cakudya, zovala, komanso pogona, alola cikondi cawo pa Mulungu kuzilala. Ena pofuna kukhutilitsa cilakolako cawo ca kugonana, amanyalanyaza miyezo ya Mulungu. (Aroma 1:26, 27) Enanso amalola anzawo kuwasonkhezela kucita zoipa pofuna kuti anzawowo aziwakonda.—Eks. 23:2.
Kodi tingalamulile bwanji zilakolako zathu? Tiyenela kuyesetsa kuika maganizo athu pa zinthu zauzimu. (Mat. 4:4) Tiyenelanso kucondelela Yehova kuti atithandize kulamulila zilakolako zathu. Cifukwa ciyani? Cifukwa iye amadziŵa zimene zili zabwino kwa ife, ndiponso amadziŵa mmene angakhutilitsile zokhumba zathu zabwino.—Sal. 145:16.
ONELELANI VIDIYO YAKUTI MUSAWONONGE MOYO WANU MWA KUKOKA FODYA. NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:
-
N’cifukwa ciyani anthu amakoka fodya?
-
Kodi kukoka fodya kungakubweletseleni mavuto otani?
-
N’cifukwa ciyani kukoka fodya n’kulakwa?—2 Akor. 7:1
-
Mungakane bwanji kukoka fodya? Nanga mungacite ciyani kuti muleke kukoka fodya?