Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Seŵenzetsani Buku la Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! Pomanga Cikhulupililo mwa Yehova Komanso mwa Yesu

Seŵenzetsani Buku la Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! Pomanga Cikhulupililo mwa Yehova Komanso mwa Yesu

Ophunzila Baibo ayenela kukhala na cikhulupililo colimba kuti akondweletse Mulungu. (Aheb. 11:6) Tingawathandize kucita zimenezi mwa kuseŵenzetsa buku lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! Bukuli limafotokoza zinthu momveka bwino, ndipo lili na malemba a mfundo zazikulu, mafunso othandiza, mavidiyo ofika munthu pa mtima, komanso zithunzi zokongola. Tikamathandiza ophunzila Baibo kukulitsa makhalidwe acikhristu komanso kukhala pa ubale wabwino na Mulungu, timamanga cikhulupililo cawo na zomangila zosagwila moto.—1 Akor. 3:12-15.

Anthu ena amaona kuti n’zosatheka kukhala pa ubwenzi na Mulungu cifukwa samuona. Conco, tiyenela kuŵathandiza kudziŵa Yehova na kum’khulupilila.

TAMBANI VIDIYO YAKUTI MANGANI CIKHULUPILILO CA OPHUNZILA MWA YEHOVA MWA KUSEŴENZETSA BUKU LAKUTI “KONDWELANI NA MOYO KWAMUYAYA!” KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:

  • N’ciyani cionetsa kuti mlongoyu anakonzekela bwino phunzilo limeneli?

  • Kodi anaseŵenzetsa bwanji mafunso owonjezela okonzedwa bwino pothandiza wophunzila kufotokozapo maganizo ake pa lemba la Yesaya 41:10, 13?

  • Kodi vidiyo na Malemba zinamukhudza bwanji wophunzila wake?

Anthu ambili salidziŵa bwino dipo, kapena saliona monga mphatso imene Mulungu anaŵapatsa. (Agal. 2:20) Conco, tiyenela kuŵathandiza kumanga cikhulupililo cawo mu nsembe ya dipo la Yesu.

TAMBANI VIDIYO YAKUTI MANGANI CIKHULUPILILO CA OPHUNZILA MWA YESU MWA KUSEŴENZETSA BUKU LAKUTI “KONDWELANI NA MOYO KWAMUYAYA!” KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:

  • N’ciyani cionetsa kuti m’baleyu anakonzekela bwino phunzilo limeneli?

  • Kodi anaseŵenzetsa bwanji zofalitsa zimene zili pa mbali yakuti “Fufuzani” kuti athandize wophunzila wake?

  • N’cifukwa ciyani n’kofunika kuti mphunzitsi azim’pemphelela wophunzilayu?