Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

“Cikondi . . . Cimayembekezela Zinthu Zonse”

“Cikondi . . . Cimayembekezela Zinthu Zonse”

Cifukwa tili na cikondi copanda dyela, timawafunila zabwino abale athu. (1 Akor. 13:4, 7) Mwacitsanzo, ngati m’bale wacita chimo ndipo wapatsidwa cilango, timakhala na ciyembekezo cakuti adzacitapo kanthu na kusintha. Timaleza nawo mtima aja ofooka m’cikhulupililo, ndipo timayesetsa kuwathandiza. (Aroma 15:1) Ngati wina wasankha kucoka mumpingo, sitileka kuyembekezela kuti tsiku lina adzabwelela.—Luka 15:17, 18.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI KUMBUKILANI MMENE CIKONDI CILILI—CIMAYEMBEKEZELA ZINTHU ZONSE, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:

  • Kodi Abineri anasintha n’kukhala wokhulupilika kwa ndani? Fotokozani

  • Kodi Davide analilandila bwanji pempho la Abineri? Nanga Yowabu analilandila motani?

  • N’cifukwa ciyani tiyenela kuwafunila zabwino abale athu?