Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

“Cikondi . . . Sicikondwela ndi Zosalungama”

“Cikondi . . . Sicikondwela ndi Zosalungama”

Akhristu oona amalola cikondi kuwatsogolela pa zocita zawo zonse. Cikondi “sicikondwela ndi zosalungama.” (1 Akor. 13:4, 6) Conco, timapewa zosangalatsa zimene zimaonetsa kuti zinthu monga zaciwelewele komanso zaciwawa n’zabwino. Komanso, sitikondwela ena akakumana na mavuto, ngakhale anthu amene anatilakwila. —Miy. 17:5.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI KUMBUKILANI MMENE CIKONDI CILILI—SICIKONDWELA NDI ZOSALUNGAMA, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:

  • Kodi Davide anamvela bwanji atadziŵa kuti Sauli na Yonatani afa?

  • Kodi Davide anaimba nyimbo yotani polila Sauli na Yonatani?

  • N’cifukwa ciyani Davide sanakondwele na imfa ya Sauli?