UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kodi Mwakonzekela Kukumana na Zacipolowe?
Pamene mapeto a dongosolo lino ayandikila, timayembekezela kuti zacipolowe, zaucigawenga, komanso nkhondo zidzawonjezeka. (Chiv. 6:4) Kodi tingakonzekele bwanji mavuto a kutsogolo?
-
Konzekelani kuuzimu: Pezani mfundo kapena nkhani za m’Baibo zimene zingalimbitse cidalilo canu mwa Yehova na gulu lake, komanso zimene zingakuthandizeni kusakhalila mbali pa zandale. (Miy. 12:5; jr 125-126 ¶23-24) Ino ndiyo nthawi yolimbitsa ubwenzi wathu na abale na alongo mumpingo.—1 Pet. 4:7, 8
-
Konzekelani kuthupi: Khalani na pulani ya mmene mungadzitetezele ngati n’zosatheka kucoka panyumba, komanso sungankoni zinthu zina zofunikila. Cina, khalani na pulani ya mmene mungathaŵile kucoka panyumba kupita ku malo otetezeka. Nthawi na nthawi, muziona ngati m’cola canu cothaŵa naco pakagwa tsoka muli zinthu zofunikila, kuphatikizapo zinthu zodzitetezela monga mamaski na magulovesi, komanso ndalama. Dziŵani mmene mungakambile na akulu, komanso tsimikizani kuti iwonso akudziŵa njila imene angakambile nanu.—Yes. 32:2; g17.5 3-7
Pamene cipolowe cili mkati, musaleke kucita zinthu zauzimu. (Afil. 1:10) Musamacoke panyumba, pokhapo ngati mukuthaŵila ku dela lina. (Mat. 10:16) Gaŵanani na ena cakudya canu na zofunikila zina.—Aroma 12:13.
ONELELANI VIDIYO YAKUTI KODI MWAKONZEKELA TSOKA LA ZACILENGEDWE? NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:
-
Kodi Yehova angatithandize bwanji pa nthawi ya matsoka?
-
Kodi tingacite ciyani kuti tikhale okonzeka?
-
Tingacite ciyani kuti tithandize amene akhudzidwa na matsoka a zacilengedwe?